REPUBLIC OF ZAMBIA
MINISTRY OF EDUCATION
MAYESO AKUDZIWA KULEMBA NDI
KUWERENGA A GIREDI 2 MU 2024
CINYANJA
KABUKU KA MPHUNZITSI KA
MALANGINZO NDI MAFUNSO
TEMU 2
SABATA LA 5
1
MALANGIZO KWA MPHUNZITSI
1. Tsiku la mayeso lisanafike, muyenera ku werengamo
m‟kabuku ka mphunzitsi ka malangizo ndi mafunso kuti
mudziwe bwino-bwino zam‟katimo. Dziwani kuti funso la
nambala 6 lifuna kuti muonetse cinthu kwa aphunzi.
Muyenera ku konzeka cinthuco tsiku la mayeso lisanafike.
2. Werenga funso liri lonse kawiri mwaluso ndiponso mosamala
momwe lalembedwera m‟kabuku ka mayeso.
3. Onetsetsa kuti aphunzi amvetsetsa funso bwino-bwino ndipo
ayankha musanapite pa funso lina.
4. Uyenera kupereka mayeso kwa aphunzi onse m‟kalasi
muzigawo A, B ndi C. Pa zigawo D E ndi F perekani mayeso kwa
aphunzi m‟modzi-m‟modzi.
5. Nthawi ya mayeso siinaikidwe, koma mayeso a mkalasi a
zigawo A, B, nd i C angatenge ola limodzi. Mayeso a m‟modzi-
m‟modzi a zigawo D, E ndi F angatenge mphindi ziwiri kapena
zitatu(2– 3 minutes) pa mphunzi ali yense.
6. Usanayambe kupereka mayeso, lemba zigawo A, B ndi C
momwe ziriri m‟kabuku ka mphunzi pa bolodi kotero kuti aphunzi
athe kulondola.
MALANGIZO KW A APHUNZI:
Tidzacita nchito. Nchitoyi ndiyamvekero, kuwerenga ndi
kulemba. Ndidzakufunsani mafunso okhudza zomwe
Ndidzanena kwa inu ndi zomwe mudza werenga. Tidzacita izi
mwaka nthawi kocepa. Mudzalemba mayankho m‟mabuku
anu. Kodi ndinu wokonzeka kuyamba?
Mphunzitsi :Onetsetsa kuti aphunzi onse ndi okonzeka kulemba
mayeso poona kuti :
Ali ndi mabuku ndi mapensulo.
Atha ku onabwino zolembedwa pa bolodi.
2
CIGAWO A : MVEKERO (PHONICS)
1. Uza aphunzi: Onani pa nambala 1 iri pa bolodi. Ndidzachula liu.
Lemba mvekero iliku ciyambi kwa liulo. Liu ndi “Kondwela ”
m k n
Yankho: m
2. Uza aphunzi: Onani pa nambala 2 iri pa bolodi. Ndidzachula
mvekero. Sankhani liu loyenelera pa mau apatsidwa pa bolodi
limene liri ndi mvekero koyambilira pa mau ndi za chula. Lemba
liu m‟mabuku anu. mvekero ndi “p”
buku pogwira gwira
Yankho: p
3. Uza aphunzi: Onani pa nambala 3 iri pa bolodi. Pali liu.
Ndidzachula silabe imene ipezeka m‟liulo. Lemba silabe limene
ndizachula. Silabe ndi bakha
khe pha kha
Yankho: kha
4. Uza aphunzi: Onani pa nambala 4 iri pa bolodi. Pali mau.
Ndidzachula masilabe awiri. Sankhani liu lomwe lipangidwa ndi
masilabe pa mau omwe apatsidwa pabolodi. Lembani liu
m‟mabuku anu. Masilabe ndi ta, ntha
nthata tantha ntheta
Yankho: nthata
3
5. Uza aphunzi: Onani pa nambala 5 iri pa bolodi. Pali liu. Lembani
nambala yamasilabe ali mu liulo m‟mabuku anu. Liu ndi nyalugwe
2 5 3
Yankho: 3
CIGAWO B: MAU (VOCABULARY)
6. Uza aphunzi: Onani pa nambala 6 iri pa bolodi. Ndidzakuonetsani
cinthu. Sankhani liu pa mau apatsidwa pa bolodi lomwe lichula
cinthuco. Lembani liu m‟mabuku anu. Cinthu ndi ici…(mpando.)
thebulo mpando bedi
Yankho: Mpando
7. Uza aphunzi: Onani pa nambala 7 iri pa bolodi. Miseu ndi yambiri.
Ngati ndi umodzi tinena kuti...... Sankhani liu loyenera pa mau
apatsidwa pa bolodi. Lembani yankho m‟mabuku anu.
kamseu mseu vimiseu
Yankho: mseu
8. Uza aphunzi: Onani pa nambala 8 iri pa bolodi. Pali ciganizo
cosatsiriza ndiposo pali mau atatu apatsidwa. Sankhani liu
loyenera kutsiriza ciganizo. Ciganizo ndi ici… Atate akonda .............
nsomba.
kumwa kubyzala kuwedza
Yankho: kuwedza
4
9. Uza aphunzi: Onani pa nambala 9 iri pa bolodi. Pali mau atatu.
Sankhani liu lofanana tanthauzo ndi liu lopatsidwa , Liu ndi kuona
kupenya kumvera kusewera
Yankho: kupenya
CIGAWO C: KULEMBA (WRITING)
10. Uza aphunzi: Onani pa nambala 10 iri pa bolodi. Pali kamzere.
Lemba liu limene ndidzachula . Liu ndi: mantha.
Yankho: mantha.
11. Uza aphunzi: Onani pa nambala 11 iri pa bolodi. Pali ciganizo ciri
ndi mau olumikidzana. Lembani ciganizoco moyenera m‟mabuku
anu posiya mipata pakati pa mau. Ciganizo ndi:
„Anthualimakumunda‟
Yankho: „Anthu alima kumunda‟
12. Uza aphunzi: Onani pa nambala 12 iri pa bolodi. Pali mpata.
Ndidzanena ciganizo kawiri. Lembani ciganizo moyenera
m‟mabuku anu . Ciganizo ndi ici: „Mwazanji wabvala delesi la
dothi‟
Yankho: „Mwazanji wabvala delesi la dothi‟
5
CIGAWO D: KUDZINDIKIRA MVEKERO (PHONEMIC AWARENESS)
Mcigawo ici, mayeso apatsidwa mwakulankhula ndi m‟modzi mmodzi
payekha.
13. Uza aphunzi: Ndidzachula liu. Ndifuna kuti undiuze mvekero
yomwe udzamva koyambilira kwa liu. Liu ndi: kumva
Yankho : k
14. Uza aphunzi : Ndidzachula liu. Ndifuna kuti undiuze mvekero
yomwe uzamva kothera kwa liu. Liu ndi: samba
Yankho : a
15. Uza aphunzi: Ndidzachula mau atatu. Ndifuna kuti undiuze liu
limene liri ndi mvekero losiyana ndi mau ena koyambira. Mau ndi
awa: mbale, mbalame, khasu
Yankho:khasu
6
CIGAWO E: MVETSO (COMPREHENSION)
Malangizo kwa mphunzitsi: Mukalibe kupatsa nkhani kwa mphunzi
kuti awerenge, onetsetsa kuti mwalemba nkhani ndi mayankho
bwino-bwino pa pepala kuti mphunzi aliyense athe kuona.
Mudzatenga mphindi zitatu pa mphunzi ali yense.
Uza mphunzi: Ndidzakupatsa mphindi imodzi kuti uwerenge
nkhani. Werenga nkhani mokweza ndi mosamala.
Ukatha kuwerenga, ndidzakufunsa mafunso awiri. Uyenera
kulemba mayankho m‟buku lako.
Nkhani ndi iyi:
Phiri ndi Zimba anapita kuchire kukapha mbewa.
Kuti apeze maenje momwe mbewa zikhala, anayatsa
moto.
Mwatsoka, moto unapitilabe kuyaka ndipo unaononga
minda ya anthu.
Phiri ndi Zimba anagwidwa ndi kuperekedwa kwa
amfumu.
Tsopano yankha mafunso awa:
16. Kodi Phiri ndi Zimba anapita kuti?
kumunda kuchire kumudzi
Yankho: kuchire
7
17. Cifukwa ninji Phiri ndi Zimba anaperekedwa kwa amfumu.?
Anaononga minda Anapita kukapha Anapita kuchire
ya anthu mbewa
Yankho: Anaononga minda ya anthu.
CIGAWO F: KUWERENGA MOSAMALA (FLUENCY)
MALANGIZO KWA MPHUNZITSI
Cigawo ici ciri ndi mamakisi atatu opatsidwa pa nambala 18, 19
ndi 20 pa pepala la makisi. Patsa mamakisi pa mau liri lonse lidza
werengedwa bwino.
18. Uza mphunzi: Ndidzakuonetsa liu. Werenga liu mokweza ndi
mofulumira. Ndidzakupatsa kanthawi kocepa (masekondi 5)
kuwerenga liu. Liu ndi: „mphepete‟
19. Uza mphunzi: Ndidzakuonetsa liu. Werenga liu mokweza ndi
mofulumira. Ndidzakupatsa ka nthawi kocepa (masekondi 5)
kuwerenga liu. Liu ndi: “ khwapula”
20. Uza mphunzi: Ndidzakuonetsa ciganizo. Werenga mokweza ndi
mofulumira. Ndidzakupatsa kanthawi kocepa (masekondi 10)
kuwerenga ciganizo. Ciganizo ndi ici:
„„Manase wadya nsomba yosasa‟‟